Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 3:11 - Buku Lopatulika

11 Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israele anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israele anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Apo mfumu Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri woti angatithandize kupempha nzeru kwa Chauta?” Mmodzi mwa atsogoleri a gulu la ankhondo la mfumu Yoramu adayankha kuti, “Aliko Elisa, mwana wa Safati, amene anali mtumiki wa Eliya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?” Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 3:11
27 Mawu Ofanana  

nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;


Ndipo anabwerera panali iye uja, natengako ng'ombe ziwiri, nazipha, naphikira nyama yake ndi zipangizo za zochitira nazo ng'ombe, napatsa anthu adye. Atatero, ananyamuka, natsata Eliya, namtumikira.


Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibe mneneri wina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?


Ndipo anachokako kunka kuphiri la Karimele; nabwera kumeneko nafika ku Samariya.


Ndipo mfumu ya Israele inati, Kalanga ife! Pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.


Nati Yehosafati, Mau a Yehova ali ndi iyeyo. Pamenepo mfumu ya Israele, ndi Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anatsikira kuli iye.


Koma anakangamira zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene anachimwitsa nazo Israele, osalekana nazo.


Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,


Ndipo Davide anafunsira kwa Mulungu, kuti, Ndikwere kodi kuyambana ndi Afilisti? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova anati kwa iye, Kwera, pakuti ndidzawapereka m'dzanja lako.


Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku.


Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.


Koma Yehosafati anati, Kulibenso kuno mneneri wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?


Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.


pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwake, niti, Kodi alipo mau ochokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo. Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni.


Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.


Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.


wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.


Ndipo atafa Mose mtumiki wa Yehova, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mnyamata wa Mose,


Pamenepo amunawo analandirako kamba wao, osafunsira pakamwa pa Yehova.


Nauka ana a Israele, nakwera kunka ku Betele, nafunsira kwa Mulungu, nati, Ayambe ndani kutikwerera pa ana a Benjamini? Ndipo Yehova anati, Ayambe ndi Yuda.


Ndipo ana a Israele anakwera nalira misozi pamaso pa Yehova mpaka madzulo; nafunsira kwa Yehova ndi kuti, Ndiyandikizenso kodi kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga? Ndipo Yehova anati, Mumkwerere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa