Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 19:34 - Buku Lopatulika

34 koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 koma mmodzi wa asilikali anamgwaza ndi nthungo m'nthiti yake, ndipo panatuluka pomwepo mwazi ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Koma mmodzi mwa asilikali aja adamubaya m'nthiti mwake ndi mkondo, ndipo nthaŵi yomweyo mudatuluka magazi ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Mʼmalo mwake, mmodzi wa asilikaliwo anamubaya Yesu ndi mkondo mʼnthiti, ndipo nthawi yomweyo munatuluka magazi ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 19:34
23 Mawu Ofanana  

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.


Ndipo m'mawa mwake, ndilo tsiku lotsatana ndi tsiku lokonzera, ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana kwa Pilato,


koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona Iye, kuti wafa kale, sanathyole miyendo yake;


Ndipo pamene adanena ichi, anaonetsa iwo manja ake ndi nthiti zake. Pamenepo ophunzira anakondwera pakuona Ambuye.


Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.


Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;


amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.


Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi;


Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo.


chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.


Mzimu, ndi madzi, ndi mwazi; ndipo iwo atatu ali mmodzi.


ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa