Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 13:1 - Buku Lopatulika

1 Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala mu Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Tsiku lomwelo padzatsegukira nyumba ya Davide ndi okhala m'Yerusalemu kasupe wa kwa uchimo ndi chidetso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku limenelo banja la Davide adzalikonzera kasupe wa madzi, kuti iwo pamodzi ndi anthu a ku Yerusalemu aŵachotsere machimo ao ndi zoipa zao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 13:1
34 Mawu Ofanana  

Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.


Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso.


pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana aakazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.


Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.


Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.


Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israele anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi machitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga chidetso cha mkazi amene akusamba.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Ndipo ndidzakupulumutsani kwa zodetsa zanu zonse, ndidzaitananso tirigu ndi kumchulukitsa, osaikiranso inu njala.


Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa chiundo cha nyumba kum'mawa; pakuti khomo lake la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kuchokera pansi pa nyumba, kumbali ya lamanja lake, kumwera kwa guwa la nsembe.


Koma kasupe kapena chitsime muli madzi, zidzakhala zoyera; koma iye amene akhudza mitembo yao adzadetsedwa.


ndipo ndidzaononga zanyanga za m'dzanja lako; ndipo sudzakhalanso nao alosi;


mabanja onse otsala, banja lililonse pa lokha, ndi akazi ao pa okha.


Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu; onse akuusenza adzadzilasa nao; ndi amitundu onse a padziko lapansi adzasonkhana kutsutsana nao.


M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.


koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:


koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.


Iye ndiye amene adadza mwa madzi ndi mwazi, ndiye Yesu Khristu; wosati ndi madzi okha, koma ndi madzi ndi mwazi. Ndipo Mzimu ndiye wakuchita umboni, chifukwa Mzimu ndiye choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa