Zekariya 13:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 “Tsiku limenelo ndidzafafaniziratu ndi maina omwe a mafano m'dziko, kotero kuti sadzaŵakumbukiranso. Ndidzachotsanso m'dziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 “Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa. Onani mutuwo |
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,