Zekariya 13:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo kudzachitika, akaneneranso wina, atate wake ndi mai wake ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wake ndi mai wake ombala adzamgwaza ponenera iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo kudzachitika, akaneneranso wina, atate wake ndi mai wake ombala adzanena naye, Sudzakhala ndi moyo, pakuti unena bodza m'dzina la Yehova; ndipo atate wake ndi mai wake ombala adzamgwaza ponenera iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Wina aliyense akadzafunabe kuti azilosa, bambo wake ndi mai wake adzamuuza kuti, ‘Sudzakhalanso ndi moyo chifukwa choti ukulosa zabodza m'dzina la Chauta.’ Motero makolo ake omwe adzambaya pamene munthuyo akulosa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya. Onani mutuwo |
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,