Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Wantchitoyo atabwera nawo abalewo m'nyumba mwa Yosefe, adaŵapatsa madzi kuti asambe mapazi ao, ndipo abulu ao aja adaŵadyetsanso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Wantchito uja anawalowetsa anthuwo mʼnyumba ya Yosefe, nawapatsa madzi kuti asambe mapazi awo. Anadyetsanso abulu awo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:24
7 Mawu Ofanana  

nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;


Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.


Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye.


Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire kunyumba yako, nutsuke mapazi ako. Ndipo Uriya anachoka kunyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu.


Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.


wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa