Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 14:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Wodwala amene wayeretsedwayo, achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe m'madzi; tsono atatero, adzakhala woyeretsedwa. Atatha zonsezo aloŵe chakumahema, koma akhale kunja kwa hema lake masiku asanu ndi aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 14:8
19 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu Uziya anali wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera, popeza ndiye wakhate; pakuti anadulidwa kunyumba ya Yehova; ndi Yotamu mwana wake anayang'anira nyumba ya mfumu naweruza anthu a m'dziko.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka kwa anthuwo, nuwapatulitse lero ndi mawa, ndipo atsuke zovala zao.


Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao.


ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa paguwa la nsembe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala iye woyera.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lake lonse la pamutu pake, ndi ndevu zake, ndi nsidze zake, inde amete tsitsi lake lonse; natsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nakhale woyera.


Ndipo wakukhayo atayeretsedwa ku kukha kwake, adziwerengere masiku asanu ndi awiri akhale a kuyeretsa kwake, natsuke zovala zake; nasambe thupi lake ndi madzi oyenda, nadzakhala woyera.


Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ake, nawasambitsa ndi madzi.


Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.


Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akuchotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zovala zao, nadziyeretse.


pamenepo mufike naye kwanu kunyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pake, ndi kuwenga makadabo ake;


chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa