Luka 7:44 - Buku Lopatulika44 Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201444 Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa44 Atatero, Yesu adacheukira mai uja, nauza Simoni kuti, “Ukumuwona maiyu? Ine ndaloŵa m'nyumba mwako muno, iwe sudandipatse madzi otsukira mapazi anga. Koma iyeyu wakhala akukhetsera misozi pa mapazi anga, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero44 Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake. Onani mutuwo |