Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake amuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa m'madzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ubwere naye Aroni ku khomo la chihema chamsonkhano, pamodzi ndi ana ake aamuna, ndipo onsewo uŵayeretse m'madzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Kenaka ubwere naye Aaroni ndi ana ake pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:4
18 Mawu Ofanana  

Ndipo uziomba nsalu yotsekera pa khomo la hema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya wopikula.


Ndipo uziike mu dengu limodzi, ndi kubwera nazo mudengu, pamodzi ndi ng'ombe yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo.


Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ake aamuna ku khomo la chihema chokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.


Ndipo anapachika pa chihema nsalu yotsekera pakhomo.


pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Atalowa ansembe asatulukenso m'malo opatulika kunka kubwalo lakunja, koma komweko aziika zovala zao zimene atumikira nazo; pakuti zili zopatulika; ndipo avale zovala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu.


Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.


Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa chihema chokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israele;


kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;


koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa chigono.


zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa