Numeri 9:5 - Buku Lopatulika Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Aisraele adachita Paska pa mwezi woyamba pa tsiku la 14, madzulo ake, m'chipululu cha Sinai. Adachita Paska monga momwe Chauta adaalamulira Mose. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. |
Ndipo ana onse a Israele anachita monga Yehova adawalamulira Mose ndi Aroni, momwemo anachita.
Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.
Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele anachitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a Israele anawachitira.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Ndipo kunali, chaka cha makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israele, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;
Taonani, ndinakuphunzitsani malemba ndi maweruzo, monga Yehova Mulungu wanga anandiuza ine, kuti muzichita chotero pakati padziko limene munkako kulilandira likhale lanulanu.
Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.
Ndipo Mosetu anali wokhulupirika m'nyumba yake yonse, monga mnyamata, achitire umboni izi zidzalankhulidwazi;
Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko.