Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:54 - Buku Lopatulika

54 Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

54 Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

54 Umu ndi m'mene adachitira Aisraele. Adachita zonse monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

54 Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:54
17 Mawu Ofanana  

Ndipo anthu anawerama, nalambira. Ndipo ana a Israele anamuka nachita monga Yehova adalamulira Mose ndi Aroni; anachita momwemo.


Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.


Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.


Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.


pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.


Monga Yehova analamula Mose, momwemo anawawerenga m'chipululu cha Sinai.


Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,


Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.


Monga Yehova adalamulira Mose, momwemo ana aakazi a Zelofehadi anachita;


Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele anachitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a Israele anawachitira.


Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa chihema ndi kukhalapo, ana a Israele anakhala m'chigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.


Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa