Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 1:53 - Buku Lopatulika

53 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

53 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa Kachisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira Kachisi wa mboni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

53 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira chihema chaumboni, kuti Mulungu asakwiyire mpingo wa Aisraele. Alevi ndiwo amene aziyang'anira chihema chaumbonicho.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

53 Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 1:53
26 Mawu Ofanana  

ndi kuti asunge udikiro wa chihema chokomanako, ndi udikiro wa malo opatulika ndi udikiro wa ana a Aroni abale ao, potumikira nyumba ya Yehova.


Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiye Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,


nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.


Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa.


koma iwe, uike Alevi asunge chihema cha mboni, ndi zipangizo zake zonse, ndi zonse ali nazo; azinyamula chihema, ndi zipangizo zake zonse; namtumikire, namange mahema ao pozungulira pa chihema.


Momwemo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose; anachita momwemo.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo moto wa ku guwa la nsembe, nuikepo chofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwachitire chowatetezera; pakuti watuluka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.


kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku gulu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya chihema cha Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;


Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'chihema cha mboni.


Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.


Mabanja a Ageresoni azimanga mahema ao pambuyo pa chihema kumadzulo.


Mabanja a ana a Kohati azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumwera.


Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja la Merari ndiye Zuriyele mwana wa Abihaili; azimanga mahema ao pa mbali ya chihema cha kumpoto.


Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la Kachisi, kum'mawa, pa khomo la chihema chokomanako kotulukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israele; koma mlendo wakuyandikizako amuphe.


Ndipo ku gawo la ana a Israele utenge munthu mmodzi mwa anthu makumi asanu, mwa ng'ombe, mwa abulu, mwa nkhosa ndi mbuzi, mwa zoweta zonse, momwemo; nuzipereke kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova.


mwa gawolo la ana a Israele Mose anatenga munthu mmodzi mwa makumi asanu, ndi zoweta momwemo, nazipereka kwa Alevi, akusunga udikiro wa chihema cha Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ake aamuna yochokera mwa ana a Israele, kuchita ntchito ya ana a Israele, m'chihema chokomanako ndi kuchita chotetezera ana a Israele; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israele, pakuyandikiza ana a Israele ku malo opatulika.


lalikira mau; chita nao pa nthawi yake, popanda nthawi yake; tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.


Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa