Numeri 1:53 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero53 Alevi nawonso, azimanga matenti awo mozungulira tenti yopatulika kuti chilango chisagwere Aisraeli onse. Ndipo Alevi aziyangʼanira ndi kusamalira tenti yopatulikayo.” Onani mutuwoBuku Lopatulika53 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa chihema cha mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira chihema cha mboni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201453 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira pa Kachisi wa mboni, kuti mkwiyo ungagwere khamu la ana a Israele; ndipo Alevi azidikira Kachisi wa mboni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa53 Koma Alevi amange mahema ao pozungulira chihema chaumboni, kuti Mulungu asakwiyire mpingo wa Aisraele. Alevi ndiwo amene aziyang'anira chihema chaumbonicho.” Onani mutuwo |
Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto.