Ahebri 11:8 - Buku Lopatulika8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Pokhala ndi chikhulupiriro, Abrahamu adamvera pamene Mulungu adamuitana kuti apite ku dziko lina limene adaamlonjeza kuti lidzakhala lake. Ngakhale sankadziŵa kumene ankapita, adapitabe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita. Onani mutuwo |