Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 11:9 - Buku Lopatulika

9 Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndi chikhulupiriro anakhala mlendo kudziko la lonjezano, losati lake, nakhalira m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, olowa nyumba pamodzi ndi iye a lonjezano lomwelo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Pokhala ndi chikhulupiriro chomwecho, ankakhala ngati mlendo m'dzikolo limene Mulungu adaamlonjeza. Ankakhala m'mahema pamodzi ndi Isaki ndi Yakobe, amene nawonso anali atalandira lonjezo lomwelo la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 11:9
22 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.


Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili mu Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.


Ndipo anankabe ulendo wake kuchokera ku dziko la kumwera kunka ku Betele, kufikira kumalo kumene kunali hema wake poyamba paja pakati pa Betele ndi Ai;


Ndipo ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako za pambuyo pako, dziko la maulendo anu, dziko lonse la Kanani likhale lako nthawi zonse: ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wako.


Ndipo Abrahamu analowa msanga m'hema wake kwa Sara, nati, Konza msanga miyeso itatu ya ufa wosalala, nuumbe, nupange mikate.


Ndipo anati kwa iye, Ali kuti Sara mkazi wako? Ndipo anati, Taonani m'hemamo.


Ndipo Abrahamu anakhala ngati mlendo masiku ambiri m'dziko la Afilisti.


Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.


Ndipo anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziwa zakusaka nyama, munthu wa m'thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m'mahema.


akupatse iwe mdalitso wa Abrahamu, iwe ndi mbeu zako pamodzi nawe: kuti ulowe m'dziko limene ukhalamo mlendo, limene Mulungu anampatsa Abrahamu.


Ndipo Labani anakomana naye Yakobo. Ndipo Yakobo anamanga hema wake m'phirimo: ndipo Labani ndi abale ake anamanga m'phiri la Giliyadi.


Ndipo Yakobo anafika kwa Isaki atate wake ku Mamure, ku Kiriyati-Ariba (ndiwo Hebroni) kumene anakhala Abrahamu ndi Isaki.


Chifukwa chuma chao chinali chambiri chotero kuti sanakhoze kukhala pamodzi; ndipo dziko lokhalamo iwo silinakhoze kuwakwanira chifukwa cha ng'ombe zao.


Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.


pokhala iwo anthu owerengeka, inde, anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;


ndiponso musamange nyumba, musafese mbeu, musaoke mipesa, musakhale nayo; koma masiku anu onse mudzakhale m'mahema; kuti mukhale ndi moyo masiku ambiri m'dziko limene mukhalamo alendo.


Momwemo Mulungu, pofuna kuonetsera mochulukira kwa olowa a lonjezano kuti chifuniro chake sichisinthika, analowa pakati ndi lumbiro;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa