Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 6:22 - Buku Lopatulika

22 Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Motero Nowa adachitadi zonse zimene Mulungu adamlamula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Nowa anachita zonse monga Mulungu anamulamulira.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 6:22
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anatenga Ismaele mwana wake ndi onse amene anabadwa m'nyumba mwake, ndi onse amene anagulidwa ndi ndalama zake, amuna onse a mwa anthu a kunyumba kwake kwa Abrahamu, nadula khungu lao tsiku lomwelo, monga Mulungu ananena naye.


Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.


Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.


zinalowa ziwiriziwiri kwa Nowa m'chingalawamo, yamphongo ndi yaikazi, monga momwe Mulungu anamlamulira Nowa.


Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.


Ndipo anayalika hema pamwamba pa Kachisi, naika chophimba cha chihema pamwamba pake; monga Yehova adamuuza Mose.


nalowa nalo likasa mu chihema, napachika nsalu yotchinga, natchinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.


Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.


nafukizapo chofukiza cha fungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose.


pakulowa iwo m'chihema chokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.


Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita.


Ndipo anauka iye, natenga kamwana ndi amake, nalowa m'dziko la Israele.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.


Chilichonse ndikuuzani, muchisamalire kuchichita; musamaonjezako, kapena kuchepsako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa