Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 9:6 - Buku Lopatulika

6 Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoze kuchita Paska tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Panali anthu ena amene anali atadziipitsa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kotero kuti sadathe kuchita nao Paska pa tsikulo. Motero adabwerera kwa Mose ndi kwa Aroni pa tsiku lomwelo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Koma ena a iwo sanathe kuchita nawo Paska pa tsiku limenelo chifukwa anali odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo. Choncho anabwera kwa Mose ndi Aaroni tsiku lomwelo,

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:6
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anati kwa mpongozi wake, Chifukwa anthu amadza kwa ine kudzafunsira Mulungu;


Tamvera mau anga tsopano, ndikupangire nzeru, ndi Mulungu akhale nawe; ukhale m'malo mwa anthu kwa Mulungu, nupite nayo milandu kwa Mulungu;


Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha.


Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake.


ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.


Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.


Iye wakukhudza mtembo wa munthu aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;


Chilamulo ndi ichi: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


Ndipo aliyense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena fupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.


ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.


Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti,


Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova.


Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi onse odetsedwa chifukwa cha akufa;


nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, pakati pa ana a Israele?


Pamenepo anamtenga Yesu kuchokera kwa Kayafa kupita ku Pretorio; koma munali mamawa; ndipo iwo sanalowe ku Pretorio, kuti angadetsedwe, koma kuti akadye Paska.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa