Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 7:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anachita Nowa monga mwa zonse anamlamulira iye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndipo Nowa adachita zonse zimene Mulungu adamlamula.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ndipo Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamulira.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 7:5
14 Mawu Ofanana  

Chotero anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.


Zimene zinalowazo, zinalowa yamphongo ndi yaikazi zamoyo zonse, monga momwe Mulungu anamlamulira iye: ndipo Yehova anamtsekera iye.


Pamenepo sindidzachita manyazi, pakupenyerera malamulo anu onse.


Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wa chihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.


Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anachita.


Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita.


Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye.


Koma Iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawachita.


Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.


Amake ananena kwa atumiki, Chimene chilichonse akanena kwa inu, chitani.


ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.


angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa