Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 9:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo anachita Paska mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo m'chipululu cha Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israele anachita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndipo Aisraele adachita Paska pa mwezi woyamba pa tsiku la 14, madzulo ake, m'chipululu cha Sinai. Adachita Paska monga momwe Chauta adaalamulira Mose.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 9:5
18 Mawu Ofanana  

Nowa anachita zonse monga Mulungu anamulamulira.


Ndipo Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamulira.


“Aisraeli onse anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni.


Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.


Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose.


Choncho Aisraeli anachita monga Yehova analamulira Mose.


Mose anawuza Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamulira.


Mose, Aaroni pamodzi ndi gulu lonse la Israeli anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose.


Choncho Mose anawuza Aisraeli kuti azichita Paska,


ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”


Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani.


“Nʼchifukwa chake Mfumu Agripa, sindinakane kumvera masomphenya wochokera kumwamba.


Mʼchaka cha makumi anayi, pa tsiku loyamba la mwezi 11, Mose anafotokozera Aisraeli zonse zimene Yehova anamulamula zokhudza iwowo.


Taonani, ndakuphunzitsani malangizo ndi malamulo monga Yehova Mulungu wanga anandilamulira kuti inuyo muwatsatire mʼdziko limene mukulowa ndi kulitengali.


Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita.


Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo.


Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa