Numeri 26:11 - Buku Lopatulika Koma sanafe ana aamuna a Kora. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma sanafe ana amuna a Kora. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe a m'banja la Kora sadafe onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma ana a Kora sanafe nawo. |
Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, ndi abale ake a nyumba ya atate wake; Akora anayang'anira ntchito ya utumiki, osunga zipata za Kachisi monga makolo ao; anakhala m'chigono cha Yehova osunga polowera;
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.
Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma. Ndinena zopeka ine za mfumu, lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.
Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Ndipo ana aamuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiyasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora.
Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna, ndi makanda ao.
ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.
Chomwecho iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano.
nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.
Ana aamuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;
ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse.
Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.