Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 26:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma ana a Kora sanafe nawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

11 Koma sanafe ana aamuna a Kora.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma sanafe ana amuna a Kora.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Komabe a m'banja la Kora sadafe onse.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:11
19 Mawu Ofanana  

Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi.


Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova.


Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi, kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.


Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu; makolo athu atiwuza zimene munachita mʼmasiku awo, masiku akalekalewo.


Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu; lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.


Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.


Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.


Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.


Imvani izi anthu a mitundu yonse; mvetserani, nonse amene mumakhala pa dziko lonse,


Wamphamvuyo, Yehova Mulungu, akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.


Ana a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu. Awa ndiwo mafuko a Kora.


Choncho anthuwo anachokadi ku matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali atatuluka nayima pamodzi ndi akazi awo, ana awo ndi makanda awo pa makomo a matenti awo.


ndipo dziko linatsekula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi nyumba zawo ndi anthu onse a Kora ndi katundu wawo yense.


Analowa mʼmanda amoyo pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. Nthaka inawatsekera ndi kuwawononga ndipo sanaonekenso.


Ndipo iye anawuza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti, “Yehova mawa mmawa adzasonyeza yemwe ndi wake ndiponso amene ndi woyera mtima. Munthuyo adzabwera pafupi ndi Iye. Munthu amene adzamusankheyo adzamusendeza pafupi.


Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;


ndi zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu mwana wa Rubeni, pamene nthaka inatsekula pakamwa pake pakati pa Aisraeli onse ndi kuwameza pamodzi ndi katundu wawo, matenti awo ndi chilichonse chawo.


Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa