Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 26:12 - Buku Lopatulika

12 Ana aamuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ana aamuna a Simeoni potsata mabanja ao ana aamuna a Simeoni anali aŵa: Nemuwele anali kholo la banja la Anemuele. Yamini anali kholo la banja la Ayamini. Yakini anali kholo la banja la Ayakini.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;

Onani mutuwo Koperani




Numeri 26:12
8 Mawu Ofanana  

Ndi ana aamuna a Simeoni: Yemuwele ndi Yamini, ndi Ohadi, ndi Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo, mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Kanani.


Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa chipinda cholowera cha Kachisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, natcha dzina lake Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, natcha dzina lake Bowazi.


Ana a Simeoni: Nemuwele, ndi Yamini, Yaribu, Zera, Shaulo,


Akulu a mbumba za makolo ao ndi awa: ana aamuna a Rubeni, woyamba wa Israele ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezironi, ndi Karimi; amenewo ndiwo mabanja a Rubeni.


Ndi ana aamuna a Simeoni ndiwo: Yemuwele, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Shaulo mwana wa mkazi wa Mkanani; amenewo ndiwo mabanja a Simeoni.


A ana a Simeoni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, owerengedwa ao, powerenga maina mmodzimmodzi, amuna onse kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;


Koma sanafe ana aamuna a Kora.


Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Shaulo, ndiye kholo la banja la Ashaulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa