Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 16:27 - Buku Lopatulika

27 Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao aamuna, ndi makanda ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna, ndi makanda ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Choncho anthuwo adachokapo pafupi ndi mahema a Kora, Datani ndi Abiramu. Pamenepo Datani ndi Abiramu adatuluka naima pakhomo pa mahema ao pamodzi ndi akazi ao, ana ao ndi makanda ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Choncho anthuwo anachokadi ku matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali atatuluka nayima pamodzi ndi akazi awo, ana awo ndi makanda awo pa makomo a matenti awo.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 16:27
9 Mawu Ofanana  

Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikulu; ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?


Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho.


Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa.


Mtima wa munthu unyada asanaonongeke; koma chifatso chitsogolera ulemu.


Chifukwa chake imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a mu Yerusalemu.


Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;


Koma sanafe ana aamuna a Kora.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa