Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 16:26 - Buku Lopatulika

26 Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Mose adauza mpingowo kuti, “Ndapota nanu, chokani pakati pa mahema a anthu oipaŵa, ndipo musakhudze chinthu chao chilichonse, kuti angakuphereni kumodzi chifukwa cha zoipa zao.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Anachenjeza gulu lonse kuti, “Khalani kutali ndi matenti a anthu oyipawa! Musakhudze kanthu kawo kalikonse, mukatero mudzawonongedwa limodzi nawo chifukwa cha machimo awo.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 16:26
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.


Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.


Thawani pakati pa Babiloni, yense apulumuke moyo wake; musathedwe m'choipa chake; pakuti ndi nthawi ya kubwezera chilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yake.


Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akulu a Israele anamtsata.


Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu.


Koma iwo, m'mene adawasansira fumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikonio.


Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa