Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.
Masalimo 7:6 - Buku Lopatulika Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ukani Yehova mu mkwiyo wanu, nyamukani chifukwa cha ukali wa akundisautsa; ndipo mugalamukire ine; mwalamulira chiweruzo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nyamukani, Inu Chauta, muli okwiya, mulimbane ndi adani anga aukali. Dzambatukani, Inu Mulungu wanga, amene mwalamula kuti chilungamo chichitike. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu; nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga. Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu. |
Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.
Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Pakuti mdani alondola moyo wanga; apondereza pansi moyo wanga; andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.
Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga, Mulungu wanga ndi Ambuye wanga.
Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele. Ukani kukazonda amitundu onse, musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga.
Monga anthu atauka, apepula loto; momwemo, Inu Ambuye, pakuuka mudzapeputsa chithunzithunzi chao.
Nyamulani mapazi anu kukapenya mapasukidwe osatha, zoipa zonse adazichita mdani m'malo opatulika.
Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; ngati chiphona chakuchita nthungululu ndi vinyo.
Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m'manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziwe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.
Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?