2 Samueli 17:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Atamva zimenezi Abisalomu ndi Aisraele onse adati, “Malangizo koma aŵa a Husai Mwarikiyu, osati a Ahitofele aja ai.” Zidatero chifukwa Chauta ndiye adaakonza kuti malangizo abwino a Ahitofele alephereke, zinthu zisamuyendere bwino Abisalomu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Abisalomu ndi ankhondo ena onse a Israeli anati, “Malangizo a Husai Mwariki ndi abwino kuposa a Ahitofele.” Pakuti Yehova anatsimikiza kutsutsa malangizo onse abwino a Ahitofele ndi cholinga choti zimuvute Abisalomu. Onani mutuwo |