Masalimo 59:5 - Buku Lopatulika5 Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele. Ukani kukazonda amitundu onse, musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndinu Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele. Ukani kukazonda amitundu onse, musachitire chifundo mmodzi yense wakuchita zopanda pake monyenga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu wa Israele. Dzambatukani kuti mulange anthu onse akunja. Musasiye ndi mmodzi yemwe mwa anthu onyengawo, ochita chiwembu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse; musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa. Onani mutuwo |
Akulu onse a ufumuwo, ndi akazembe ndi akalonga, mandoda, ndi ziwanga, anapangana kukhazika lemba lachifumu, ndi kuikapo choletsa cholimba, kuti aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m'dzenje la mikango.