Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 59:4 - Buku Lopatulika

4 osawapatsa chifukwa ine, athamanga nadzikonza. Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 osawapatsa chifukwa ine, athamanga nadzikonza. Galamukani kukomana nane, ndipo penyani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 ngakhale sindidalakwe, anthuwo akuthamanga kukonzekera nkhondo. Dzambatukani, mudzandithandize, ndipo muwone.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo. Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 59:4
13 Mawu Ofanana  

chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.


Adani anga asandikondwerere ine monyenga; okwiya nane kopanda chifukwa asanditsinzinire.


Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga, Mulungu wanga ndi Ambuye wanga.


Galamukani, mugoneranji, Ambuye? Ukani, musatitaye chitayire.


Mudzaononga iwo akunena bodza; munthu wokhetsa mwazi ndi wachinyengo, Yehova anyansidwa naye.


Kodi adzapulumuka ndi zopanda pake? Gwetsani anthu mumkwiyo, Mulungu.


pakuti mapazi ao athamangira zoipa, afulumira kukhetsa mwazi.


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao.


Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu a milandu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.


miyendo yao ichita liwiro kukhetsa mwazi;


Ndipo Yonatani analankhula ndi Saulo atate wake movomereza Davide, nanena naye, Mfumu asachimwire mnyamata wake Davide; chifukwa iyeyo sanachimwire inu, ndipo ntchito zake anakuchitirani zinali zabwino ndithu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa