Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 59:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Onani, iwo akubisalira moyo wanga, anthu oopsa agwirizana kuti andithire nkhondo. Ngakhale sindidachite choipa kapena kuchimwa konse, Inu Chauta,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Onani momwe iwo akundibisalira! Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane; osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 59:3
18 Mawu Ofanana  

amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo.


Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,


Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.


Amemezana, alalira, atchereza mapazi anga, popeza alindira moyo wanga.


Ondida kopanda chifukwa achuluka koposa tsitsi la pamutu panga; ofuna kunditha, ndiwo adani anga monama, ali ndi mphamvu. Pamenepo andibwezetsa chosafunkha ine.


Mau a oipa abisalira mwazi; koma m'kamwa mwa olungama muwalanditsa.


Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo.


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


Koma chitero, kuti mau olembedwa m'chilamulo chao akwaniridwe, kuti, Anandida Ine kopanda chifukwa.


Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.


Ndipo Saulo analankhula kwa Yonatani mwana wake, ndi anyamata ake onse kuti amuphe Davide.


Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.


Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.


Nati iye, Chifukwa ninji mbuye wanga amalondola mnyamata wake? Pakuti ndachitanji? Kapena m'dzanja langa muli choipa chotani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa