ndi Zekariya, ndi Aziyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, ndi Eliyabu, ndi Maaseiya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuimbira mwa Alimoti;
Masalimo 6:1 - Buku Lopatulika Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, ndipo musandilange muukali wanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, ndipo musandilange m'kukali wanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, musandikalipire ndi kundidzudzula, musapse mtima ndi kundilanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu. |
ndi Zekariya, ndi Aziyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, ndi Eliyabu, ndi Maaseiya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuimbira mwa Alimoti;
ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi Azaziya, ndi azeze akuimbira mwa Seminiti, kutsogolera maimbidwe.
Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.
Pakufuula ine mundiyankhe, Mulungu wa chilungamo changa; pondichepera mwandikulitsira malo. Ndichitireni chifundo, imvani pemphero langa.
Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso padziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.
Pakuti sindidzatsutsana kunthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
Usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; pakuti Ine ndili ndi iwe; pakuti Ine ndidzathetsa mitundu yonse kumene ndinakuingitsirako iwe, koma sindidzakuthetsa iwe; koma ndidzakulangiza ndi chiweruziro, ndipo sindidzakusiya konse wosalangidwa.