Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 38:1 - Buku Lopatulika

1 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu, ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Yehova, musandidzudzule ndi mkwiyo wanu, ndipo musandilange moopsa m'mtima mwanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Chauta musandikwiyire ndi kundidzudzula. Musapse mtima ndi kundilanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yehova musandidzudzule mutapsa mtima kapena kundilanga muli ndi ukali.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 38:1
11 Mawu Ofanana  

Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, ndipo musandilange muukali wanu.


Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu! Fulumirani kundithandiza, Yehova.


Mkwiyo wanu utsamira pa ine, ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.


Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.


M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa chikhalire ndidzakuchitira chifundo, ati Yehova Mombolo wako.


Yehova, mundilangize, koma ndi chiweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.


Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.


Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.


Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani. Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa