Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 37:40 - Buku Lopatulika

40 Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa; Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa, pakuti amathawira kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 37:40
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.


Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse, landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;


Pondifika ine ochita zoipa kudzadya mnofu wanga, inde akundisautsa ndi adani anga, anakhumudwa iwo nagwa.


Iye asunga mafupa ake onse; silinathyoke limodzi lonse.


Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.


Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wa makamu adzatchinjiriza Yerusalemu; Iye adzatchinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.


ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.


Taonani, Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m'ng'anjo yotentha yamoto, nadzatilanditsa m'dzanja lanu, mfumu.


Nebukadinezara ananena, nati, Alemekezedwe Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, amene anatuma mthenga wake, napulumutsa atumiki ake omkhulupirira Iye, nasanduliza mau a ine mfumu, napereka matupi ao kuti asatumikire kapena kulambira mulungu wina yense, koma Mulungu waowao.


Pamenepo mfumu inakondwera kwambiri, niwauza atulutse Daniele m'dzenje. Momwemo anamtulutsa Daniele m'dzenje, ndi pathupi pake sipadaoneke bala, popeza anakhulupirira Mulungu wake.


Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa