Masalimo 41:5 - Buku Lopatulika Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma adani anga ondifunira zoipa, amati, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti, kuti aiŵalike?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?” |
Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.
Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo; ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.
Mundibwerere ine, ndi kundichitira chifundo; mpatseni mtumiki wanu mphamvu yanu, ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.