Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 38:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Anthu ofunafuna moyo wanga, amanditchera misampha. Ofuna kundipweteka amalankhula zondiwononga, tsiku lonse amangolingalira zondichita chiwembu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo, oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga; tsiku lonse amakonza zachinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 38:12
18 Mawu Ofanana  

Iye anandichotsera abale anga kutali, ndi odziwana nane andiyesa mlendo konse.


Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.


Oipa ananditchera msampha; koma sindinasokere m'malangizo anu.


Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.


Mundisunge ndisagwe mumsampha ananditcherawo, ndisakodwe m'makwekwe a iwo ochita zopanda pake.


Ndaiwalika m'mtima monga wakufa, ndikhala monga chotengera chosweka.


Pakuti salankhula zamtendere, koma apangira chiwembu odekha m'dziko.


Athe nzeru nachite manyazi iwo akufuna moyo wanga; abwezedwe m'mbuyo nasokonezeke iwo akundipangira chiwembu.


Adani anga andinenera choipa, ndi kuti, adzafa liti, ndi kutayika dzina lake?


Pakuti alendo andiukira, ndipo oopsa afunafuna moyo wanga; sadziikira Mulungu pamaso pao.


Pakuti changu cha pa nyumba yanu chandidya; ndi zotonza za iwo otonza Inu zandigwera ine.


Diso langa lapuwala chifukwa cha kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; nditambalitsira manja anga kwa Inu.


Abale onse a wosauka amuda; nanga mabwenzi ake kodi satanimphirana naye? Awatsata ndi mau, koma kuli zii.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa