Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 38:11 - Buku Lopatulika

11 Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga; ndipo anansi anga aima patali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga; ndipo anansi anga aima patali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Abwenzi anga ndi anzanga omwe amandiimira kutali, chifukwa cha matenda anga. Achibale anga nawonso amandipewa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga; anansi anga akhala kutali nane.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 38:11
12 Mawu Ofanana  

Pakuti andizinga agalu, msonkhano wa oipa wanditsekereza; andiboola m'manja anga ndi m'mapazi anga.


Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse, inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa; iwo akundipenya pabwalo anandithawa.


Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa, odziwana nane akhala kumdima.


Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa.


Anachotsedwa ku chipsinjo ndi chiweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wake? Pakuti walikhidwa kunja kuno; chifukwa cha kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.


Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.


Ndipo pamenepo anamgwira Iye, napita naye, nalowa m'nyumba ya mkulu wa ansembe. Koma Petro anatsata kutali.


Ndipo omdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, anaima kutali, naona zinthu izi.


Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa