Masalimo 20:1 - Buku Lopatulika Yehova akuvomereze tsiku la nsautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova akuvomereze tsiku la nsautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto. Mulungu wa Yakobe akuteteze. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze. |
Ndingakhale ndiyenda pakati pa nsautso, mudzandipatsa moyo; mudzatambasula dzanja lanu pa mkwiyo wa adani anu, ndipo dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba padziko lonse lapansi.
ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiye iwo akufuna Inu.
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.
Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,