Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.
Masalimo 2:4 - Buku Lopatulika Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wokhala m'mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta amene amalamulira kumwambako akungoŵaseka ndi kuŵanyoza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo. |
Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.
Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.
Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.
Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe; taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.
Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?