Masalimo 15:1 - Buku Lopatulika Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Chauta, kodi ndani angathe kukhala m'Nyumba mwanu? Ndani angathe kukhala pa phiri lanu loyera? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera? |
Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.
Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso.
Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.
Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,
Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.