Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 15:2 - Buku Lopatulika

2 Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndi munthu amene amayenda mosalakwa, amene amachita zolungama nthaŵi zonse, amene amalankhula zinthu ndi mtima woona.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 15:2
23 Mawu Ofanana  

Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye; iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe, ndipo salumbira monyenga.


Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.


Wolungama woyenda mwangwiro, anake adala pambuyo pake.


Woyenda mwangwiro adzapulumuka; koma wokhota m'mayendedwe ake adzagwa posachedwa.


Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa;


Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.


Kodi adzati, Nyumba ya Yakobo iwe, Mzimu wa Yehova waperewera kodi? Izi ndi ntchito zake kodi? Mau anga samchitira zokoma kodi, iye amene ayenda choongoka?


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


koma m'mitundu yonse, wakumuopa Iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.


koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki;


Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukakamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?


Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.


Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.


musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,


amene mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu, anachita chilungamo, analandira malonjezano, anatseka pakamwa pa mikango,


Ngati mudziwa kuti ali wolungama, muzindikira kuti aliyensenso wakuchita chilungamo abadwa kuchokera mwa Iye.


iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.


Tiana, munthu asasokeretse inu; iye wakuchita cholungama ali wolungama, monga Iyeyu ali wolungama:


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa