Masalimo 143:4 - Buku Lopatulika Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine; mtima wanga utenga nkhawa m'kati mwanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake mtima wanga wafooka m'kati mwanga, mumtima mwangamu mukuchita mantha. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho mzimu wanga ukufowoka mʼkati mwanga; mʼkati mwanga, mtima wanga uli ndi nkhawa. |
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
Penyani kudzanja lamanja ndipo muone; palibe wondidziwa; pothawirapo pandisowa; palibe mmodzi wosamalira moyo wanga.
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.
Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.