Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 55:5 - Buku Lopatulika

5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera, ndipo zoopsetsa zandikuta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Mantha ndi kunjenjemera zandidzera, ndipo zoopsetsa zandikuta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mantha andifikira, ndipo ndikunjenjemera, mantha aakulu andigwira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mantha ndi kunjenjemera zandizinga; mantha aakulu andithetsa nzeru.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 55:5
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa.


Ndikangokumbukira ndivutika mtima, ndi thupi langa lichita nyaunyau.


Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.


Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.


M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.


Mulungu wanga, moyo wanga udziweramira m'kati mwanga; chifukwa chake ndikumbukira Inu m'dziko la Yordani, ndi mu Aheremoni, m'kaphiri ka Mizara.


Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.


Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.


Ndipo adzadzimangira m'chuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzachita manyazi, ndi mitu yao yonse idzachita dazi.


Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa