Masalimo 140:2 - Buku Lopatulika amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iwo amalingalira mumtima mwao kuti achite zoipa, amautsa nkhondo nthaŵi zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse. |
Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.
Ndipo anditchera misampha iwo akufuna moyo wanga; ndipo iwo akuyesa kundichitira choipa alankhula zoononga, nalingirira zonyenga tsiku lonse.
Pakuti onani, alalira moyo wanga; amphamvu andipangira chiwembu, osachimwa, osalakwa ine, Yehova,
Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?
Pakuti asendera nao mtima wao wakunga ng'anjo ya mkate, pokhala alikulalira; wootcha mkate wao agona usiku wonse, m'mawa iyaka ngati moto wa malawi.
Mwa iwe watuluka wina wolingalira choipa chotsutsana ndi Yehova, ndiye phungu wopanda pake.