Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo; nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka.
Masalimo 127:2 - Buku Lopatulika Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda. |
Ndipo udzalimbika mtima popeza pali chiyembekezo; nudzafunafuna, ndi kugona mosatekeseka.
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Kuti okondedwa anu alanditsidwe, pulumutsani ndi dzanja lanu lamanja, ndipo mutivomereze.
Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.
Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.
Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.