Mlaliki 1 - Buku LopatulikaZa pansi pano nzachabe 1 Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya mu Yerusalemu. 2 Zachabechabe, ati Mlaliki; zachabechabe zonse ndi chabe. 3 Kodi ntchito zake zonse munthu asauka nazo zimpindulira chiyani? 4 Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse. 5 Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako. 6 Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake. 7 Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso. 8 Zinthu zonse zilemetsa; munthu sangathe kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva. 9 Chomwe chinaoneka chidzaonekanso; ndi chomwe chinachitidwa chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano. 10 Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife. 11 Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai. 12 Ine Mlaliki ndinali mfumu ya Israele mu Yerusalemu. 13 Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimachitidwa pansi pa thambo; ntchito yovuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo. 14 Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima. 15 Chokhotakhota sichingaongokenso; ndipo choperewera sichingawerengedwe. 16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso. 17 Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima. 18 Pakuti m'nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe aenjezera chidziwitso aenjezera zowawa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi