Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 1:16 - Buku Lopatulika

16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Mumtima mwangamu ndinkati, “Ndatola nzeru zambiri, kupambana onse amene ankalamulira ku Yerusalemu kale. Ndaphunzira zambiri zaluntha ndi zanzeru.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.”

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 1:16
20 Mawu Ofanana  

Koma sindinakhulupirire mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.


Ndipo nzeru ya Solomoni inaposa nzeru za anthu onse akum'mawa, ndi nzeru zonse za ku Ejipito.


Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebanoni kufika nayo ku nyanja, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzachita chifuniro changa, kumapatsa banja langa zakudya.


Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.


Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israele, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wake.


Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.


Ndikumbukira nyimbo yanga usiku; ndilingalira mumtima mwanga; mzimu wanga unasanthula.


Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.


Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.


Ndinakula chikulire kupambana onse anali mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; ndipo nzeru yanganso inakhala nanebe.


Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.


amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira tsindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.


Mfumu inanena, niti, Suyu Babiloni wamkulu ndinammanga, akhale pokhala pachifumu, ndi mphamvu yanga yaikulu uoneke ulemerero wachifumu wanga?


Koma chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa chabwino ndi choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa