Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 1:10 - Buku Lopatulika

10 Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Ichi ndiye nchatsopano?” Iyai, chidaalipo kale, ifenso kukadalibe nkomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti, “Taona! Ichi ndiye chatsopano?” Chinalipo kale, kalekale; chinalipo ife kulibe.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 1:10
10 Mawu Ofanana  

Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.


Chomwe chinaoneka chidzaonekanso; ndi chomwe chinachitidwa chidzachitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.


Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale.


Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sangathe kulimbana ndi womposa mphamvu.


Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu mu Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.


Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.


Ndipo monga momwe Yane ndi Yambere anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana nacho choonadi; ndiwo anthu ovunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pachikhulupiriro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa