Masalimo 112:7 - Buku Lopatulika Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazika, wokhulupirira Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Saopa akamva zoyipa zimene zachitika; mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova. |
Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza.
Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.
Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye; ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.
Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, anayankha, nati kwa mfumu Nebukadinezara, Sikufunika kuti tikuyankheni pa mlandu uwu.
Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi mapanduko, musaopsedwa; pakuti ziyenera izi ziyambe kuchitika; koma mathedwe sakhala pomwepo.
Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.
Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.
Chifukwa chake, limbikani mtima, amuna inu; pakuti ndikhulupirira Mulungu, kuti kudzatero monga momwe ananena ndi ine.