Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;
Masalimo 112:1 - Buku Lopatulika Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake. |
Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;
Aleluya. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.
Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero ali nacho chidziwitso chokoma; chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.
Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma; pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.
kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.
Angakhale wochimwa achita zoipa zambirimbiri, masiku ake ndi kuchuluka, koma ndidziwitsadi kuti omwe aopa Mulungu naopa pamaso pake adzapeza bwino;
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.
pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.