Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Hoseya 10:3 - Buku Lopatulika

Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Posachedwa anthuwo adzanena kuti, “Tilibe mfumu tsopano chifukwa sitidamvere Chauta. Komabe mfumuyo ikadatichitira chiyani ife?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu chifukwa sitinaope Yehova. Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”

Onani mutuwo



Hoseya 10:3
14 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wake chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi mu Samariya.


Kuthawira kwa Yehova nkokoma koposa kukhulupirira akulu.


amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?


amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize ntchito yake kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israele uyandikire, udze kuti tiudziwe!


Momwemo adzakuchitirani Betele, chifukwa cha choipa chanu chachikulu; mbandakucha mfumu ya Israele idzalikhika konse.


Ndipo Samariya, mfumu yake yamwelera ngati thovu pamadzi.


Iye sadzabwerera kunka kudziko la Ejipito, koma Asiriya adzakhala mfumu yake, popeza anakana kubwera.


Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'mizinda yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?


Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamchotsanso mu ukali wanga.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Tsono ufuulitsa chifukwa ninji? Palibe mfumu mwa iwe kodi? Watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?


Pamenepo anafuula iwowa, Chotsani, Chotsani, mpachikeni Iye! Pilato ananena nao, Ndipachike mfumu yanu kodi? Ansembe aakulu anayankha, Tilibe mfumu koma Kaisara.


Koma mukaumirirabe kuchita choipa, mudzaonongeka, inu ndi mfumu yanu yomwe.