Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 13:10 - Buku Lopatulika

10 Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'mizinda yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ili kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'midzi yako yonse? Ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Inu munkati, ‘Tipatseni mfumu ndi atsogoleri.’ Nanga tsopano mfumu yanuyo, yoti ikulanditseni, ili kuti? Nanga atsogoleri anuwo, oti akutchinjirizeni, ali kuti?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse? Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti, amene iwe unanena za iwo kuti, ‘Patseni mfumu ndi akalonga?’

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 13:10
26 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, atamva Aisraele onse kuti Yerobowamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisraele onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma fuko lokha la Yuda.


Koma mfumu ya Asiriya anampeza Hoseya alikuchita chiwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Ejipito, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asiriya, monga akachita chaka ndi chaka; chifukwa chake mfumu ya Asiriya anamtsekera, nammanga m'kaidi.


Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya; aonongeka amitundu m'dziko lake.


Akondwere Israele mwa Iye amene anamlenga; ana a Ziyoni asekere mwa mfumu yao.


Inu ndinu mfumu yanga, Mulungu; lamulirani chipulumutso cha Yakobo.


Koma Mulungu ndiye mfumu yanga kuyambira kale, wochita zakupulumutsa pakati padziko lapansi.


Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova; ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele.


Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.


Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israele, Mfumu yanu.


Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa mizinda yako, Yuda iwe.


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,


Pakuti tsopano adzati, Tilibe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzatichitira chiyani?


Koma Ine ndiye Yehova Mulungu wako chichokere m'dziko la Ejipito, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine.


Analonga mafumu, koma sikunachokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golide wao, kuti akalikhidwe.


Ndipo Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse; tsiku lomwelo Yehova adzakhala Iye yekha, ndi dzina lake ilo lokha.


Natanaele anayankha Iye, Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu mfumu ya Israele.


Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa